Chichewa Module 2 Summary
MUTU 1: Kaphunzitsidwe ka kumva ndi kuyankhula
Mitu ya ntchito ya kumva ndi kuyankhula:
i. malonje
ii. zouzidwa
iii. zilapi
iv. nthano
v. ndakatulo
vi. nyimbo
Njira zophunzitsira maluso a kumva ndi kuyankhula
i. Kuchita sewero:
ii. Kusonyeza
iii. Kuyesana
iv. Ntchito ya m’magulu
v. Kukambirana (kalasi yonse kapena mphunzitsi ndi ophunzira)
vi. Kufunsa ndi kuyankha mafunso
vii. Kufotokoza
MUTU 2. Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka ndakatulo ndi nyimbo m’sitandade 5 mpaka 8.
Ndakatulo
Ndakatulo ndi maganizo olembedwa mwachidule m’mdime imodzi kapena zingapo.
Nyimbo
Nyimbo ndi maganizo omwe amanenedwa kudzera m’kuimba
Mitundu ya ndakatulo
i. Zampululira:
Zomwe mawu akomalizira samveka mofanana
ii. Zamapasa:
Zomwe mawu akomalizira amamveka mofanana
Mitundu ya nyimbo
Zachisoni
Zothokoza
Zodzudzula
Zachisangalalo
Kufunika kwa ndakatulo ndi nyimbo
Kupititsa patsogolo chikumbumtima
Kuti ophunzira aziganiza mozama
Kuti ophunzira adziwe katchulidwe kabwino ka mawu monga kutsitsa kapena kukweza
Kuti ophunzira aziyankhula pagulu mopanda manyazi
Kuti ophunzira adziwe zambiri zachiyankhulo
Ntchito za ndakatulo ndi nyimbo
Kuphunzitsa
Kulangiza
Kudzudzula
Kuthokoza
Kuthandiza kusunga chikhalidwe cha makolo
Kusangalatsa
Zipangizo zophunzitsira ndakatulo ndi nyimbo
ng’oma
wenzulo
badza
chitoliro
Ndondomeko yophunzitsira ndakatulo ndi nyimbo
Choyamba, uzani ophunzira alakatule ndakatulo kapena ayimbe nyimbo yomwe akuyidziwa
kale
Kachiwiri, funsani ophunzira kulongosola zomwe ndakatulo kapena nyimbo ikunena
Kachitatu, werengani ndakatulo yomwe muphunzitse (powerenga mutsatire kukweza
kapena kutsitsa kwa mawu; kuwonetsa chisoni; kusonyeza chisangalalo; kugwedeza thupi
ngakhalenso kuvina kumene)
Kachinayi, funsani ophunzira kuwerenga ndakatulo ndipo mukhale tcheru kumvetsera
momwe ophunzira akutchulira mawu
Kachisanu, kambiranani ndi ophunzira zomwe ndakatuloyo/nyimboyo ikunena.
Kachisanu ndi chimodzi, pemphani ophunzira kuloweza ndime imodzi kapena zingapo
(Langizo: sibwino kuumiriza ophunzira kuloweza ndakatulo/nyimbo
MUTU 3: Kaphunzitsidwe ka kukonzekera kuwerenga
Kuwerenga ndi kuzindikira ndi kutchula zolemba kuti tanthauzo limveke bwino
Kufunika kwa kuwerenga
Kuthandiza ophunzira kupeza zochita zina
Kuthandiza ophunzira omwe akuphunzira paokha
Kutola nzeru zambiri kuchokera m’mabuku osiyanasiyana
Kuti aziwerenga zikwangwani, malangizo ndi zidziwitso paokha
Kukonzekera ntchito yodzagwira mtsogolo
Kuthandiza pophunzira maphunziro ena
Zomwe mphunzitsi angachite ndi ophunzira pa phunziro la kukonzekera kuwerenga
Kuloza kumaso ndi kumbuyo kwa buku
Kugwira buku moyenera osati mozondotsa
Kutsekula buku moyenera
Kuloza poyambira ndi pothera pa mawu
Kupenya patsamba kuyambira kumanzere kupita kumanja
Kuloza mawu m’chiganizo
Kuyika buku pa mpata oyenera
Kusiyanitsa zinthu zosiyanasiyana
Kufananitsa zinthu zosiyanasiyana
Njira zothandizira kudziwa malire amawu
Kutchula mawu amodziamodzi m’chiganizo uku akuwomba m’manja akatchula mawu
amodzi
Kugwiritsa ntchito zala ndi mipata yomwe ili pakati pa zala. Chala chilichonse chiziyimira
mawu amodzi pamene mpata pakati pa zala uyimira mpata womwe uyenera kukhalapo
pakati pa mawu
Pogwiritsa ntchito chithunzi (makadi a mawu) monga:
Amayi apit lero
a
MUTU 4 Njira zophunzitsira ndi kuyesera kuyamba kuwerenga m’sitandade 1
1. Njira yomwe ophunzira amatsata maliwu a malembo
Aphunzitsi amatsata maliwu a malembo omwe ali m’chiyankhulo chomwe
chikuphunzitsidwa monga /a/ /n/ /i/ /m/
Ngati ophunzira adziwa lembo ndi liwu lake, ndiye kuti angathe kuwerenga yekha komanso
kulemba mawu osiyanasiyana mosavuta.
2. Njira yotsata maphatikizo a malembo
Mphunzitsi amaphunzitsa ophunzira kuwerenga pogwiritsa ntchito maphatikizo a malembo
monga mba + le = mbale, a + ba + ba = ababa
3. Njira yotsata mawu
Mphunzitsi amayamba kuphunzitsa mawu omwe iwo akuwadziwa kale monga maina a
zinthu zomwe amaziona kunyumba kwawo, monga chitseko, mbiya, mbuzi, galu, nkhuku,
ng’ombe.
Zithunzi ndi zinthu zenizeni zimayenera zikhalepo pogwiritsa ntchito njirayi.
Kenako mphunzitsi amawaphunzitsa ophunzirawo mawu ena.
4. Njira yotsata ziganizo
Mphunzitsi amayamba kuphunzitsa ophunzira ziganizo zomwe amazidziwa kale
Ziganizo zimaperekedwa ndi ophunzirawo powafunsa mafunso monga:
i. Pobwera kusukulu mwaona chiyani?
ii. Munagwira ntchito yanji lero kunyumba?
Mphunzitsi amalemba pa bolodi zomwe mwana wayankha
Kenako amawathandiza ophunzirawo kuwerenga chiganizocho
Mutu 5 Zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
Kufunika kwa zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
Mphunzitsi amafotokoza mfundo mosavuta
Ophunzira amamvetsa msanga phunziro
Zimapatsa chidwi ophunzira
Ophunzira saiwala msanga zomwe aphunzira
Zimathandiza kusunga nthawi pophunzitsa
Zitsanzo za zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
i.. makadi
Amapangidwa kuchokera ku mapepala olimba kapena zikuto
Ntchito yake
Kulembapo malembo, maphatikizo ndi mawu
Kagwiritsidwe ntchito kake
Ophunzira kutola khadi ndikuwerenga
Kuchita masewero osiyanasiyana monga opanga mawu ndi maphatikizo
monga: a ndi ta ndi te kupanga mawu oti atate
Mphunzitsi kulangiza khadi la lembo, phatikizo kapena mawu kuti ophunzira awerenge
ii.. matchati
Awa ndi mapepala akulu
Ntchito yake
kulembapo malembo, maphatikizo, mawu, ziganizo ndi ndakatulo
kujambulapo chithunzi ndikulemba mawu okhudzana ndi chithunzicho
Zina zoyenera kuchita zokhudza matchati
kudula mzere m’mbali mwa tchati kuti liwoneke lokongola ndilopatsa chidwi
khomani tchati m’kalasi mwanu mukatha kuphunzitsa kuti ophunzira aziwerenga pa nthawi
yawoyawo.
iii.. Mabolodi ofewa:
Onani zitsanzo zomwe zili pakhomo lolowera mu HALL, komanso ku admin pa reception,
m’maofesi ndi m’kalasi mwanu.
Ntchito yake
Kupachikapo zinthu zosiyanasiyana zothandiza powerenga, ntchito yomwe ophunzira
analemba mwaluso ndi maina a ophunzira omwe akhoza bwino.
Ngati mulibe mabolodi ofewa, gwiritsani ntchito mphasa, mkeka, bulangete
iv.. Alifabeti fulizi
Awa ndi malembo omwe amathandiza ophunzira kudziwa kuwerenga
Pamakhala lembo lalikulu ndi laling’ono monga Aa, Dd, Mm
Pa lembo lililonse pamajambuilidwa chithunzi chogwirizana nd liwu loyamba la dzina la
chithunzicho
Pachikani alifabeti fulizi pakhoma mukatha kuphunzitsira kuti ophunzira aziwerenga paokha
v.. Bokosi la kanema
Limapangidwa kuchokera ku katoni, ndodo ziwiri ndi zithunzi zojambulidwa pa pepala
lalitali.
Ntchito yake
Limathandiza powerenga kapena kufotokoza nthano
Kagwiritsidwe ntchito kake
Potolozani (rotate) ndodozo kuti zithunzi ziziyenda ngati kanema.
vi.. Kansalu kacheya (fulanelo galafu)
Aka ndi kansalu kacheya
Ngati palibe gwiritsani ntchito bulangeti, thaulo la kubafa kapena chiguduli.
Ntchito yake
Kupachikapo makadi olembapo mawu ndi zithunzi
Kuwerengetsa mawu ndi ziganizo
vii.. Timabolodi
Timapangidwa kuchokera ku matabwa, dongo ndi katoni ndi utoto (paint)
Ntchito yake
Kulembapo malembo, maphatikizo mawu ndi ziganizo zazifupi
Ubwino wake
Zomwe zalembedwapo zikhoza kufufutidwa kuti palembedwe zina
Timakhala nthawi yayitali.
viii. Zidole
Zimapangidwa kuchokera ku dongo, udzu kapena nsalu
Ntchito yake
Zimathandiza pophunzitsa ophunzira a m’makalasi ang’onoang’ono powerenga nthano,
kapena nkhani
Zimachititsa phunziro kukhala lopatsa chidwi ophunzira.
ix.. Zithunzi
Mutha:
Kujambula nokha, kudula kuchokera mu nyuzipepala, magazine kapenaa kalendala yakale
Kutenga zithunzi zofalitsa mauthenga osiyanasiyana.
Ubwino wake
Ophunzira amamvetsa zomwe akuwerenga
Ophunzira amakhala ndi chidwi ndi phunziro
MUTU 6: Kaphunzitsidwe ka kuwerenga nkhani kapena nthano
Ndondomeko yophunzitsira nkhani kapena nthano msitandade 3 mpaka 8
Kambiranani ndi ophunzira zomwe akuona pa chithunzi chomwe chili m’buku la ophunzira
koyambirira kwa nkhani/ nthano iliyonse
Ophunzira awerenge mokweza mawu ovuta opezeka m’nkhani/m’nthano yomwe
awerenge. Kenako muwonetse ophunzira mawu ovutawo pa makadi ndipo ophunzira
awerenge.
Ophunzira awerenge mwakachetechete nkhani/nthano yonse
Kambiranani ndi ophunzira matanthauzo a mawu ovuta molingana ndi momwe mawuwo
agwiritsidwa ntchito m’nkhani/m’nthano
Ophunzira ayankhe mosalemba mafunso ochokera m’nkhani/m’nthano yomwe awerenga
Ophunzira achite ntchito monga kusanja mawu.
Thandizani ophunzira ndikuchonga ntchito yawo
Potsiriza kambiranani ndi ophunzira zolakwa zawo ndipo kenaka ophunzira akonze zolakwa
zawo
Njira zothandizira kumvetsa nkhani/nthano m’sitandade 3 mpaka 8
Kupanga kalozera wa mfundo zikuluzikulu
Kulosera nkhani
Kudzifunsa mafunso
Kupanga mafunso
Kulosera mathero a nkhani
Kugwiritsa ntchito zomwe akuzidziwa kale
Zofunika mphunzitsi kudziwiratu asanaphunzitse kuwerenga nthano.
Mawu ovuta ndi katchulidwe kake
Matanthauzo a mawu ovuta
Nthani/nthano yomwe afuna kuphunzitsa
Mafunso oyenera kufunsa pa nkhani/nthano poonjezera omwe ali kale m’buku la ophunzira
Mayankho a mafunso omwe ali m’buku la ophunzira
Zizindikiro za m’kalembedwe pamene ophunzira akuwerenga nkhani/nthano.
MUTU 7: Kuwerenga mabuku oonjezera
Kufunika kowerenga mabuku oonjezera
Kuti ophunzira akulitse nkhokwe yawo ya mawu
Kupeza chisangalalo
Kupezamo nzeru zambiri
Kupititsa patsogolo luso lowerenga mofulumira molondola ndi mosadodoma
Kukulitsa khalidwe lokonda kuwerenga mabuku
Kukonzekeretsa ophunzira ntchito yodzagwira m’tsogolo
Zitsanzo za mabuku oonjezera
Nyuzipepala
Magazini
Mabuku akale
Mabuku a nthano/nkhani zifupizifupi
Nkhani zolemba ophunzira
Ndondomeko yophunzitira kuwerenga mabuku oonjezera
Kuyala mabuku pa tebulo kapena malo oyenera
Kuuza ophunzira kusankha buku lomwe afuna kuwerenga
Ophunzira kuwerenga buku lomwe asankha
Kufunsa ophunzira mafunso pa buku lomwe awerenga
Kubwereketsa ophunzira mabuku kuti akawerenge kwawo
Ena mwa mafunso omwe ophunzira angafunsidwe akawerenga mabuku oonjezera ndi monga
awa:
Tchulani mutu wa nkhani yomwe mwawerenga.
Kodi nkhaniyo ndiyosangalatsa?
Nkhani ikukamba za anthu ati?
Kodi mwaphunzirapo chiyani pa nkhani yomwe mwawerenga?
Nkhaniyo ikuchitikira kuti? Etc
Mutu 8: Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka kulemba mwaluso ndi kulemba zidziwitso
Ndondomeko yphunzitsira kulemba mwaluso
Poyamba ophunzira abwereze kuwerenga mokweza ndime ziwiri za m’buku la ophunzira
Kachiwiri jambulani mizere ndi kulemba mwaluso malembo ndi mawu.
Kachitatu ophunzira m’modzi awerenge zomwe zalembedwa pabolodi
Kachinayi ophunzira alembe malembo ndi mawu m’mizere m’makope mwawo
Kachisanu thandizani ophunzira ndi kuchonga zomwe alemba.
Pomaliza, ophunzira abwereze kulemba malembo ndi mawu pabolodi.
Mitundu ya zidziwitso
Zochenjeza monga: Chenjerani ndi akuba
Zolangiza monga: Pewani kuchita chiwerewere
Zophunzitsa monga: Kupewa kuposa kuchiza
Zodziwitsa monga: Mlatho waung’ono patsogolo
Ndondomeko yophunzitsira kulemba zidziwitso
Poyamba ophunzira akambirane m’magulu zidziwitso zosiyanasiyana zimene akuzidziwa.
Kachiwiri thandizani ophunzira kuyika zidziwitso m’magulu molingana ndi ntchito yomwe
zikugwira (mtundu)
Kachitatu sonyezani ophunzira kalembedwe ka zidziwitso
Kachinayi ophunzira ajambule zidziwitso zosiyanasiyana m’magulu mwawo
Pomaliza gulu lililonse liwonetse ntchito yawo kwa kalasi lonse
MUTU 9: Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka kulemba lembetso
Kufunika kwa lembetso
Kuthandiza ophunzira:
Kulemba mawu ndi ziganizo pamtima
Kudziwa kulemba zizindikiro zam’kalembedwe
Kulimbikitsa maluso akumva ndi kulemba nthawi imodzi
Kutha kulemba mwaluso
Kutha kulemba mwachangu komanso molondola
Kukhala ndi maziko a ntchito yam’tsogolo monga ulembi
Kumvetsera mwatcheru zomwe wina akukamba kapena kumvetsera
Ndondomeko yophunzitsira lembetso
Bwerezani kulemba ndime yomwe ophunzira alembe
Kambiranani mawu achilendo ndi zizindikiro za m’kalembedwe
Werengani ndime yonse kamodzi ophunzira akungomvetsera
Werengani kachigawo kalikonse kawiri ophunzira akulemba
Werenganinso ndime yonse kamodzi kuti ophunzira akonze zolakwa zawo
Chongani ntchito ya ophunzira
Kambiranani ndi ophunzira zomwe alakwa
Kenako ophunzira akonze zolakwazo
Njira zochongera lembetso
1. Mphunzitsi kuchonga yekha
Ubwino wake
Mumadziwa mavuto a ophunzira aliyense ndi momwe mungamuthandizire
Mumadziwa ngati ophunzira amva kapena ayi
Ophunzira amkhutira ndi ntchito yochongedwa ndi mphunzitsi wawo
Makolo amakondwera ndi ntchito yochongedwa ndi mphunzitsi wa ana awo
Kuyipa kwake
Ndi ntchito yofunika nthawi yambiri
Ophunzira amalandira ntchito yawo mochedwa
2. Ophunzira kuchongerana ntchito mosinthana
Ubwino wake
Ntchito imachongedwa mofulumira
Ophunzira amakhalaa ndi mwayi ophunzira luso lochonga
Kuyipa kwake
Ena amachonga mokonderana
Ena satha kuwona zolakwa za anzawo
Ophunzira sakhutira ndi ntchito yochongedwa ndi anzawo
Makolo sakhutira ndi ntchito yochongerana ophunzira okhaokha
3. Kusankha ophunzira ena kuchonga ntchito ya anzawo
Ubwino wake
Osankhidwawo amaphunzira luso lochonga
Amakonzekera ntchito yam’tsogolo monga ya uphunzitsi
Kuyipa kwake
Si onse amachonga moyenera
Amane sanasankhidwe kuchonga nawo amakhumudwa
Ophunzira ena amanyoza anzawo
4. Ophunzira aliyense adzichongere yekha
Ubwino wake
Ophunzira aliyense amadziwa zofooka zake
Ophunzira amawonetsa kukhulupirika pochonga ntchito ya anzawo kumanso ya iwo eni
Kuyipa kwake
Si ophunzira onse amakhulupirika pochonga ntchito yawo
Zizindikiro zomwe mungagwiritse ntchito pochonga lembetso
Kutseka mzere kunsi kwa mawu olakwa
Kuyika chizindikiro choti ophunzira wasiya mawu ena
Kuzunguliza pamene ophunzira walakwitsa
MUTU 10: Kaphunzitsidwe ka kulemba chimangirizo
Mfundo zoyenera kuganizira polemba chimangirizo.
Pezani mutu omwe uli ndi mfundo zambiri
Lembani padera chikonzekero cha mfundo (draft/rough work) zomwe mukufuna kulemba.
Gwiritsani ntchito nsinjiro zachiyankhulo, koma zisakhale koyambirira kwa ndime ndipo
zisatsangane
Musagwiritse ntchito mawu olaula ndi achipongwe
Lembani malembo ooneka bwino
Ndondomeko yophunzitsira chimangirizo mu sitandade 3 ndi 4
Pezani zitsanzo za ndondomeko m’buku la mphunzitsi la sitandade 3 ndi 4.
Ndondomeko yophunzitsira chimangirizo mu sitandade 5 mpaka 8
Lembani mutu wa chimangirizo pabolodi
Kambiranani ndi ophunzira mfundo zazikuluzikulu pa mutu omwe wasankhidwandi
kuzisanja mu ndondomeko yoyenera
Kambiranani ndi ophunzira chitsanzo cha momwe angalembere chimangirizo pogwiritsa
ntchito mafunso.
Ophunzira alembe chimangirizo pogwiritsa ntchito mutu omwe mwapereka potsatira
mafunso owatsogolera.
Onani ntchito ya ophunzira ndi kuwathandiza pamene akulemba
Pomaliza tengani ntchito ya ophunzira kuti mukachonge.
MUTU 11: Kaphunzitsidwe ka kulemba kalata
Ndondomeko yophunzitsira kulemba kalata ya ntchito m’sitandade 5 mpaka 8
Funsani ophunzira ngati adalembapo kapenaa kuwonapo kalata yantchito.
Pachikani tchati ya chitsanzo cha kalata yantchito ndipo mukambirane ndi ophunzira
magawo a kalata monga keyala, tsiku, komwe kalata ikupita, malonje, thunthu, mathero.
Ophunzira alembe kalata yantchito pa mutu omwe mwapereka ndipo mphunzitsi ayendere
ndi kuthandiza ophunzira.
Pomaliza, ophunzira ena angspo awerenge kalata zawo ndipo mutenge makope awo kuti
mukachonge.
MUTU 12: Kaphunzitsidwe ka kulemba nkhani, nthano ndi sewero
Mfundo zoyenera kutsata polemba nkhani, nthano ndi sewero
Kusankha mutu wosavuta kupeza mfundo zosangalatsa zikatambasulidwa
Mutu ukhale wolingana ndi nzeru za ophunzira
Osalemba mawu achipongwe kapena olaula
Malembo azikkhala owerengeka
Chiganizo chilichonse chizikhala ndi mfundo yayikulu
Mfundo yayikulu itambasulidwe mokwanira
Ndime ziziyalidwa mu dongosolo loyenera kutsatira kufunika kwake
Pa ndime iliyonse pazikhala mfundo yoomba mkota
Nthano, nkhani ndi sewero zizikhala zosangalatsa
Kuwerenga ndi kukonza zomwe zalembedwa
MUTU 13: Kaphunzitsidwe ka kugwiritsa ntchito malamulo a chiyankhulo
Zomwe zimalepheretsa ophunzira akupulayimale kugwiritsa ntchito malamulo achiyankhulo
moyenera.
Kusagwiritsa ntchito zipangizo pophunzitsa
Kusagwiritsa ntchito zipangizo zosiyanasiyana pophunzitsa
Kusakhala ndi chizoloweza chowerenga mabuku owonjezera nzeru
Chizolowezi choyankhula ziyankhulo zachilendo monga chingerezi
Chizolowezi choyankhula ziyankhulo zam’madera
Kusakhala ndi chidwi pa phunziroli
Njira zomwe zingathandize kuthetsa mavuto omwe ophunzira amakumana nawo pogwiritsa
ntchito malamulo a chiyankhulo.
Kugwiritsa ntchito zipangizo zoyeneraa pophunzitsa
Kutsata njira zosiyanasiyana pophunzitsa
Kukhala ndi chizolowezi chowerenga mabuku oonjezera
Kuzoloweraa kuyankhula Chichewa
Kukhala ndi chizolowezi choyankhula Chichewa chithyakuka
Kukhala ndi chidwi pa phunziroli
MUTU 14: Kaphunzitsidwe ka ndagi/zilapi
Mitundu ya ndagi
Ndagi zonena zinthu zamoyo
Ndagi zonena zinthu zopanda moyo
Kufunika kwa ndagi.
Kuthandiza kuganiza mozama
Kubweretsa chisangalalo
Kusunga chikhalidwe chamakolo
Mutu 15: Kaphunzitsidwe ka mikuluwiko
Kufunika kwa mikuluwiko
Imakometsa nkhani
Imathandiza poyankhula mozimbaitsa
Imagwiritsidwa ntchito pa milandu
Imathandiza kuganiza mozama
Imaphunzitsa ndi kulimbikitsa makhalidwe abwino
Imaphunzitsa chiyambi cha zinthu
Imapititsa patsogolo chikhalidwe cha makolo
Imathandiza kuyanjanitsa anthu omwe asemphana mawu (akukangana)
Ndondomeko yophunzitsira mikuluwiko
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akudziwako zokhudza mikuluwiko
Kupereka tanthauzo la mkuluwiko
Kupereka zitsanzo za mikuluwiko
Kupereka matanthauzo ya mikuluwiko yomwe yaperekedwa ngati zitsanzo
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kulemba matanthauzo a mikuluwiko
Kuuza ophunzira kukachita kafukufuku wa zitsanzo zina za mikuluwiko.
Mutu 16: Kaphunzitsidwe ka nthano
Kufunika kwa nthano
Kusangalatsa
Kuphunzitsa
Kudziwitsa
Ndondomeko yophunzitisira nthano
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akudziwako zokhudza nthano
Kupereka tanthauzo la nthano
Kupereka chitsanzo cha nthano
Kunena nthano
Kufotokoza kapekedwe ka nthano
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kuyankha mafunso ndi kupereka phunziro lopezeka
mu nthano kapena kukamba za apangankhani, malo nthawi ndi zina.
Kuuza ophunzira kukachita kafukufuku wa zitsanzo zina za nthano.
Mutu 17: Kaphunzitsidwe ka sewero
Kufunika kwa phunziro la sewero
Kuyankhula pagulu mopanda manyazi
Kusangalatsa
Kupititsa patsogolo luso lomvetsera mwatcheru
Kuphunzitsa
Kuthandiza kuganiza mozama
Kukonzekera ntchito yodzagwira mtsogolo
Kudzudzula
Kidziwitsa anthu zinthu zosiyanasiyana
Ndondomeko yophunzitsira sewero
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akuzidziwa zokhudza sewero/zisudzo
Kupereka chitsanzo cha sewero
Kufotokoza kufunika kwa sewero
Kufotokoza zopezeka m’sewero
Kuchita sewero
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kuchita sewero, kufotokoza za atengambali,
makhalidwe awo, komamso phunziro lopezeka mu sewero.
Kuchita kafukufuku wa masewero ena.
Mutu 18: Kaphunzitsidwe ka kuzukuta (analysis of) nyimbo ndi ndakatulo
Mfundo zoyenera kutsatira pozukuta nyimbo kapena ndakatulo
Ndani akuyankhula?
Akuti chiyani?
Akuyankhula ndi yani?
N’chifukwa chiyani akuyankhula zimenezi?
Kodi woyankhulayo ndi wosangalala, wachisoni, wokhumudwa?
Ndi mfundo yayikulu iti yomwe ikupezeka mu nyimbo kapena ndakatulo
Zipangizo za nsetso (mawu apadera omwe amagwiritsidwa ntchito monga: mpeputso,
msemphano, voko, m’malere)
Njira zophunzitsira kumvetsa nkhani/nthano yomwe ophunzira awerenga.
1. Njira yolosera pogwiritsa ntchito mutu ndi zithunzi za nkhani/nthano
Ophunzira amafunsidwa mafunso pa mutu ndi zithunzi ndipo iwo amapereka maganizo awo
nkhani/nthano isanawerengedwe, monga mukuganizo kuti nkhaniyi ikamba zotani?
Lembani pa bolodi zina mwa zomwe ophunzira akuganiza.
Chepetsani mafunso oti “mukuonapo chiyani” pachithunzipa.
Njirayi imapereka chidwi kwa ophunzira chofuna kuwerenga nkhani.
2. Njira yolosera mathero a nkhani
Tikawerenga kapena kumvetsera ndime kapena gawo la nkhani timatha kulosera mathero a
nkhani.
Timafunsa mafunso monga: Kodi nkhaniyi itha bwanji malingana ndi ndime y(z)omwe
tawerenga kapena kumvetsera?
3. Njira yopanga chithunzithunzi cha nkhani
Tikamawerenga kapena kumvetsera nkhani timatha kupanga chithunzithunzi m’maganizo
mwathu cha zimene zikuchitika, malo kapena nthawi yomwe nkhani ikuchitika ndi omwe
akuchita.
Izi zimathandiza kumvetsa ndi kukumbukira zomwe zawerengedwa.
4. Njira yofotokozanso nkhani
Uku ndikufotokoza nkhani m’mawu athuathu momwe tayiwerengera ndi kuyimvetsera.
5. Njira yopanga mafunso
Timapanga mafunso tikatha kuwerenga nkhani.
Mafunso amakhala okhudza ampangankhani, malo, mfundo zikuluzikulu ndi phunziro
lopezeka m’nkhaniyo.
6. Njira yodzifunsa mafunso
Njirayi timadzifunsa mafunso pamene tikuwerenga nkhani.
Titha kufunsa mafunso tikawerenga mizere ingapo kapena ndime imodzi, monga: Kodi
munthuyu amakatani kumsikaku?
7. Njira younika mpangankhani
M’njirayi timapeza yemwe akuyankhula m’nkhani, zomwe akuyankhula ndi zifukwa zake,
gawo lomwe akutenga, ubale ndi ampangankhani ena komanso malo ndi nthawi yochitikira
nkhani.
8. Njira ya kalozera wa mfundo zikuluzikulu
Njirayi timayang’ana mfundo zikuluzikulu zomwe zikupezeka m’nkhani kapena m’macheza.
9. Njira yolumikiza zomwe akudziwa kale ndi zimene aphunzire.
M’njirayi timagwiritsa ntchito zomwe tikudziwa kale kuti timvetse nkhani yomwe tiwerenge.
Chi Mod 2 sum
MUTU 1: Kaphunzitsidwe ka kumva ndi kuyankhula
Njira zophunzitsira maluso a kumva ndi kuyankhula
(mitu ya ntchito ya kumva ndi kuyankhula: malonje, zouzidwa zilapi, nthano, ndakatulo,
nyimbo)
Kuchita sewero:
Kusonyeza
Kuyesana
Ntchito ya m’magulu
Kukambirana (kalasi yonse/mphunzitsi ndi ophunzira)
Kufunsa ndi kuyankha mafunso
Kufotokoza
MUTU 2. Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka ndakatulo ndi nyimbo m’sitandade 5 mpaka 8.
Tanthauzo la:
Ndakatulo
Maganizo olembedwa mwachidule m’mdime imodzi kapena zingapo.
Nyimbo
Maganizo omwe amanenedwa kudzera m’kuimba
Mitundu ya ndakatulo
Zampululira:
Zomwe mawu akomalizira samveka mofanana
(Pezani zitsanzo m’mabuku a ophunzira a standard 5 mpaka 8)
Zamapasa:
Zomwe mawu akomalizira amamveka mofanana
Mitundu ya nyimbo
Zachisoni
Zothokoza
Zodzudzula
Zachisangalalo
Kufunika kwa ndakatulo ndi nyimbo
Kupititsa patsogolo chikumbumtima (enhancing memory of what is learnt)
Kuti ophunzira aziganiza mozama
Kuti ophunzira adziwe katchulidwe kabwino ka mawu monga kutsitsa kapena kukweza
Kuti ophunzira aziyankhula pagulu mopanda manyazi
Kuti ophunzira adziwe zambiri zachiyankhulo
Etc
Ntchito za ndakatulo ndi nyimbo
Kuphunzitsa
Kulangiza
Kudzudzula
Kuthokoza
Kuthandiza kusunga chikhalidwa
Kusangalatsa
Etc
Zipangizo zophunzitsira ndakatulo ndi nyimbo
ng’oma
wenzulo
badza
chitoliro
Etc
Ndondomeko yophunzitsira ndakatulo ndi nyimbo
Choyamba, uzani ophunzira alakatule ndakatulo kapena ayimbe nyimbo yomwe akuyidziwa
kale
Kachiwiri, funsani ophunzira kulongosola zomwe ndakatulo kapena nyimbo ikunena
Kachitatu, werengani ndakatulo yomwe muphunzitse (powerenga mutsatire kukweza
kapena kutsitsa kwa mawu; kuwonetsa chisoni; kusonyeza chisangalalo; kugwedeza thupi
ngakhalenso kuvina kumene)
Kachinayi, funsani ophunzira kuwerenga ndakatulo ndipo mukhale tcheru kumvetsera
momwe ophunzira akutchulira mawu
Kachisanu, kambiranani ndi ophunzira zomwe ndakatuloyo/nyimboyo ikunena.
Kachisanu ndi chimodzi, pemphani ophunzira kuloweza ndime imodzi kapena zingapo
(Langizo: sibwino kuumiriza ophunzira kuloweza ndakatulo/nyimbo
MUTU 3: Kaphunzitsidwe ka kukonzekera kuwerenga
Tanthauzo la kuwerenga: Kuzindikira ndi kutchula zolemba kuti tanthauzo limveke bwino
Kufunika kwa kuwerenga
Kuthandiza ophunzira kupeza zochita zina (for pleasure)
Kuthandiza ophunzira omwe akuphunzira paokha
Kutola nzeru zambiri kuchokera m’mabuku osiyanasiyana
Kuti aziwerenga zikwangwani, malangizo ndi zidziwitso paokha
Kukonzekera ntchito yodzagwira mtsogolo
Kuthandiza pophunzira maphunziro ena
Zomwe mphunzitsi angachite ndi ophunzira pa phunziro la kukonzekera kuwerenga
Kuloza kumaso ndi kumbuyo kwa buku
Kugwira buku moyenera osati mozondotsa
Kutsekula buku moyenera
Kuloza poyambira ndi pothera pa mawu
Kupenya patsamba kuyambira kumanzere kupita kumanja
Kuloza mawu m’chiganizo
Kuyika buku pa mpata oyenera
Kusiyanitsa zinthu zosiyanasiyana
Kufananitsa zinthu zosiyanasiyana
Njira zothandizira kudziwa malire amawu
Kutchula mawu amodziamodzi m’chiganizo uku akuwomba m’manja akatchula mawu
amodzi
Kugwiritsa ntchito zala ndi mipata yomwe ili pakati pa zala. Chala chilichinse chiziyimira
mawu amodzi pamene mpata pakati pa zala uyimira mpata womwe uyenera kukhalapo
pakati pa mawu
Pogwiritsa ntchito chithunzi monga:
Amayi apit lero
a
MUTU 4 Njira zophunzitsira ndi kuyesera kuyamba kuwerenga
Pali zosoyanasiyana zomwe mphunzitsi angagwiritse ntchito pophunzitsa kuyamba kuwerenga
m’sitandade 1.
Njira yomwe ophunzira amatsata maliwu a malembo
Aphunzitsi amatsata maliwu a malembo omwe ali m’chiyankhulo chomwe
chikuphunzitsidwa monga /a/ /n/ /i/ /m/
Ngati ophunzira adziwa lembo ndi liwu lake, ndiye kuti angathe kuwerenga yekha komanso
kulemba mawu osiyanasiyana mosavuta.
Njira yotsata maphatikizo amalembo
Mphunzitsi amaphunzitsa ophunzira kuwerenga pogwiritsa ntchito maphatikizo a malembo
monga mba + le = mbale, a + ba + ba = ababa
Njira yotsata mawu
Mphunzitsi amayamba kuphunzitsa mawu omwe iwo akuwadziwa kale monga maina a
zinthu zomwe amaziona kunyumba kwawo, monga chitseko, mbiya, mbuzi, galu, nkhuku,
ng’ombe.
Zithunzi ndi zinthu zenizeni zimayenera zikhalepo pogwiritsa ntchito njirayi.
Kenako mphunzitsi amawaphunzitsa ophunzirawo mawu ena.
Njira yotsata ziganizo
Aphunzitsi amayamba kuphunzitsa ophunzira ziganizo zomwe amazidziwa kale
Ziganizo zimaperekedwa ndi ophunzirawo powafunsa mafunso monga:
iii. Pobwera kusukulu mwaona chiyani?
iv. Munagwira ntchito yanji lero kunyumba?
Mphunzitsi amalemba pa bolodi zomwe mwana wayankha
Kenako amawathandiza ophunzirawo kuwerenga chiganizocho
MUTU 5: Zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
Kufunika kwa zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
Mphunzitsi amafotokoza mfundo mosavuta
Ophunzira amamvetsa msanga phunziro
Zimapatsa chidwi ophunzira
Ophunzira saiwala msanga zomwe aphunzira
Zimathandiza kusunga nthawi pophunzitsa
Zitsanzo za zipangizo zophunzitsira, zophunzirira ndi zoyesera kuwerenga
makadi
Amapangidwa kuchokera ku mapepala olimba kapena zikuto
Ntchito yake
Kulembapo malembo, maphatikizo ndi mawu
Kagwiritsidwe ntchito kake
Ophunzira kutola khadi ndikuwerenga
Kuchita masewero osiyanasiyana monga opanga mawu ndi maphatikizo
monga: a ndi ta ndi te kupanga mawu oti atate
Mphunzitsi kulangiza khadi la lembo, phatikizo kapena mawu kuti ophunzira awerenge
matchati
Awa ndi mapepala akulu
Ntchito yake
kulembapo malembo, maphatikizo, mawu, ziganizo ndi ndakatulo
kujambulapo chithunzi ndikulemba mawu okhudzana ndi chithunzicho
Zina zoyenera kuchita zokhudza matchati
kudula mzere m’mbali mwa tchati kuti liwoneke lokongola ndilopatsa chidwi
khomani tchati m’kalasi mwanu mukatha kuphunzitsa kuti ophunzira aziwerenga pa nthawi
yawoyawo.
Mabolodi ofewa:
Onani zitsanzo zomwe zili pakhomo lolowera mu HALL, komanso ku admin pa reception,
m’maofesi ndi m’kalasi mwanu.
Ntchito yake
Kupachikapo zinthu zosiyanasiyana zothandiza powerenga, ntchito yomwe ophunzira
analemba mwaluso ndi maina a ophunzira omwe akhoza bwino.
Ngati mulibe mabolodi ofewa, gwiritsani ntchito mphasa, mkeka, bulangete
Alifabeti fulizi
Awa ndi malembo omwe amathandiza ophunzira kudziwa kuwerenga
Pamakhala lembo lalikulu ndi laling’ono monga Aa, Dd, Mm
Pa lembo lililonse pamajambuilidwa chithunzi chogwirizana nd liwu loyamba la dzina la
chithunzicho
Pachikani alifabeti fulizi pakhoma mukatha kuphunzitsira kuti ophunzira aziwerenga paokha
Bokosi la kanema
Limapangidwa kuchokera ku katoni, ndodo ziwiri ndi zithunzi zojambulidwa pa pepala
lalitali.
Ntchito yake
Limathandiza powerenga kapena kufotokoza nthano
Kagwiritsidwe ntchito kake
Potolozani (rotate) ndodozo kuti zithunzi ziziyenda ngati kanema.
Kansalu kacheya (fulanelo galafu)
Aka ndi kansalu kacheya
Ngati palibe gwiritsani ntchito bulangeti, thaulo la kubafa kapena chiguduli.
Ntchito yake
Kupachikapo makadi olembapo mawu ndi zithunzi
Kuwerengetsa mawu ndi ziganizo
Timabolodi
Timapangidwa kuchokera ku matabwa, dongo ndi katoni ndi utoto (paint)
Ntchito yake
Kulembapo malembo, maphatikizo mawu ndi ziganizo zazifupi
Ubwino wake
Zomwe zalembedwapo zikhoza kufufutidwa kuti palembedwe zina
Timakhala nthawi yayitali.
Zidole
Zimapangidwa kuchokera ku dongo, udzu kapena nsalu
Ntchito yake
Zimathandiza pophunzitsa ophunzira a m’makalasi ang’onoang’ono powerenga nthano,
kapena nkhani
Zimachititsa phunziro kukhala lopatsa chidwi ophunzira.
Zithunzi
Mutha:
Kujambula nokha, kudula kuchokera mu nyuzipepala, magazine kapenaa kalendala yakale
Kutenga zithunzi zofalitsa mauthenga osiyanasiyana.
Ubwino wake
Ophunzira amamvetsa zomwe akuwerenga
Ophunzira amakhala ndi chidwi ndi phunziro
-----------------------------------------------------------------------------------------------------------
MUTU 6: Kaphunzitsidwe ka kuwerenga nkhani kapena nthano
Ndondomeko yophunzitsira nkhani kapena nthano msitandade 3 mpaka 8
Kambiranani ndi ophunzira zomwe akuona pa chithunzi chomwe chili m’buku la ophunzira
koyambirira kwa nkhani/ nthano iliyonse
Ophunzira awerenge mokweza mawu ovuta opezeka m’nkhani/m’nthano yomwe
awerenge. Kenako muwonetse ophunzira mawu ovutawo pa makadi ndipo ophunzira
awerenge.
Ophunzira awerenge mwakachetechete nkhani/nthano yonse
Kambiranani ndi ophunzira matanthauzo a mawu ovuta molingana ndi momwe mawuwo
agwiritsidwa ntchito m’nkhani/m’nthano
Ophunzira ayankhe mosalemba mafunso ochokera m’nkhani/m’nthano yomwe awerenga
Ophunzira achite ntchito monga kusanja mawu.
Thandizani ophunzira ndikuchonga ntchito yawo
Potsiriza kambiranani ndi ophunzira zolakwa zawo ndipo kenaka ophunzira akonze zolakwa
zawo
Njira zothandizira kumvetsa nkhani/nthano m’sitandade 3 mpaka 8
Kupanga kalozera wa mfundo zikuluzikulu
Kulosera nkhani
Kudzifunsa mafunso
Kupanga mafunso
Kulosera mathero a nkhani
Kugwiritsa ntchito zomwe akuzidziwa kale
Zofunika mphunzitsi kudziwiratu asanaphunzitse kuwerenga nthano.
Mawu ovuta ndi katchulidwe kake
Matanthauzo a mawu ovuta
Nthani/nthano yomwe afuna kuphunzitsa
Mafunso oyenera kufunsa pa nkhani/nthano poonjezera omwe ali kale m’buku la ophunzira
Mayankho a mafunso omwe ali m’buku la ophunzira
Zizindikiro za m’kalembedwe pamene ophunzira akuwerenga nkhani/nthano
----------------------------------------------------------------------------------------------------------
MUTU 7: Kuwerenga mabuku oonjezera
Kufunika kowerenga mabuku oonjezera
Kuti ophunzira akulitse nkhokwe yawo ya mawu
Kupeza chisangalalo
Kupezamo nzeru zambiri
Kupititsa patsogolo luso lowerenga mofulumira molondola ndi mosadodoma
Kukulitsa khalidwe lokonda kuwerenga mabuku
Kukonzekeretsa ophunzira ntchito yodzagwira m’tsogolo
Zitsanzo za mabuku oonjezera
Nyuzipepala
Magazini
Mabuku akale
Mabuku a nthano/nkhani zifupizifupi
Nkhani zolemba ophunzira
Ndondomeko yophunzitira kuwerenga mabuku oonjezera
Kuyala mabuku pa tebulo kapena malo oyenera
Kuuza ophunzira kusankha buku lomwe afuna kuwerenga
Ophunzira kuwerenga buku lomwe asankha
Kufunsa ophunzira mafunso pa buku lomwe awerenga
Kubwereketsa ophunzira mabuku kuti akawerenge kwawo
Ena mwa mafunso omwe ophunzira angafunsidwe akawerenga mabuku oonjezera ndi monga
awa:
Tchulani mutu wa nkhani yomwe mwawerenga.
Kodi nkhaniyo ndiyosangalatsa?
Nkhani ikukamba za anthu ati?
Kodi mwaphunzirapo chiyani pa nkhani yomwe mwawerenga?
Nkhaniyo ikuchitikira kuti? Etc
Mutu 8: Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka kulemba mwaluso ndi kulemba zidziwitso
Ndondomeko yphunzitsira kulemba mwaluso
Poyamba ophunzira abwereze kuwerenga mokweza ndime ziwiri za m’buku la ophunzira
Kachiwiri jambulani mizere ndi kulemba mwaluso malembo ndi mawu.
Kachitatu ophunzira m’modzi awerenge zomwe zalembedwa pabolodi
Kachinayi ophunzira alembe malembo ndi mawu m’mizere m’makope mwawo
Kachisanu thandizani ophunzira ndi kuchonga zomwe alemba.
Pomaliza, ophunzira abwereze kulemba malembo ndi mawu pabolodi.
Mitundu ya zidziwitso
Zochenjeza monga: Chenjerani ndi akuba
Zolangiza monga: Pewani kuchita chiwerewere
Zophunzitsa monga: Kupewa kuposa kuchiza
Zodziwitsa monga: Mlatho waung’ono patsogolo
Ndondomeko yophunzitsira kulemba zidziwitso
Poyamba ophunzira akambirane m’magulu zidziwitso zosiyanasiyana zimene akuzidziwa.
Kachiwiri thandizani ophunzira kuyika zidziwitso m’magulu molingana ndi ntchito yomwe
zikugwira (mtundu)
Kachitatu sonyezani ophunzira kalembedwe ka zidziwitso
Kachinayi ophunzira ajambule zidziwitso zosiyanasiyana m’magulu mwawo
Pomaliza gulu lililonse liwonetse ntchito yawo kwa kalasi lonse
MUTU 9: Kaphunzitsidwe ndi kayesedwe ka kulemba lembetso
Kufunika kwa lembetso
Kuthandiza ophunzira:
Kulemba mawu ndi ziganizo pamtima
Kudziwa kulemba zizindikiro zam’kalembedwe
Kulimbikitsa maluso akumva ndi kulemba nthawi imodzi
Kutha kulemba mwaluso
Kutha kulemba mwachangu komanso molondola
Kukhala ndi maziko a ntchito yam’tsogolo monga ulembi
Kumvetsera mwatcheru zomwe wina akukamba kapena kumvetsera
Ndondomeko yophunzitsira lembetso
Bwerezani kulemba ndime yomwe ophunzira alembe
Kambiranani mawu achilendo ndi zizindikiro za m’kalembedwe
Werengani ndime yonse kamodzi ophunzira akungomvetsera
Werengani kachigawo kalikonse kawiri ophunzira akulemba
Werenganinso ndime yonse kamodzi kuti ophunzira akonze zolakwa zawo
Chongani ntchito ya ophunzira
Kambiranani ndi ophunzira zomwe alakwa
Kenako ophunzira akonze zolakwazo
Njira zochongera lembetso
Mphunzitsi kuchonga yekha
Ubwino wake
Mumadziwa mavuto a ophunzira aliyense ndi momwe mungamuthandizire
Mumadziwa ngati ophunzira amva kapena ayi
Ophunzira amkhutira ndi ntchito yochongedwa ndi mphunzitsi wawo
Makolo amakondwera ndi ntchito yochongedwa ndi mphunzitsi wa ana awo
Kuyipa kwake
Ndi ntchito yofunika nthawi yambiri
Ophunzira amalandira ntchito yawo mochedwa
Ophunzira kuchongerana ntchito mosinthana
Ubwino wake
Ntchito imachongedwa mofulumira
Ophunzira amakhalaa ndi mwayi ophunzira luso lochonga
Kuyipa kwake
Ena amachonga mokonderana
Ena satha kuwona zolakwa za anzawo
Ophunzira sakhutira ndi ntchito yochongedwa ndi anzawo
Makolo sakhutira ndi ntchito yochongerana ophunzira okhaokha
Kusankha ophunzira ena kuchonga ntchito ya anzawo
Ubwino wake
Osankhidwawo amaphunzira luso lochonga
Amakonzekera ntchito yam’tsogolo monga ya uphunzitsi
Kuyipa kwake
Si onse amachonga moyenera
Amane sanasankhidwe kuchonga nawo amakhumudwa
Ophunzira ena amanyoza anzawo
Ophunzira aliyense adzichongere yekha
Ubwino wake
Ophunzira aliyense amadziwa zofooka zake
Ophunzira amawonetsa kukhulupirika pochonga ntchito ya anzawo kumanso ya iwo eni
Kuyipa kwake
Si ophunzira onse amakhulupirika pochonga ntchito yawo
Zizindikiro zomwe mungagwiritse ntchito pochonga lembetso
Kutseka mzere kunsi kwa mawu olakwa
Kuyika chizindikiro choti ophunzira wasiya mawu ena
Kuzunguliza pamene ophunzira walakwitsa
MUTU 10: Kaphunzitsidwe ka kulemba chimangirizo
Mfundo zoyenera kuganizira polemba chimangirizo. Zina mwa izo ndi:
Pezani mutu omwe uli ndi mfundo zambiri
Lembani padera chikonzekero cha mfundo (draft/rough work) zomwe mukufuna kulemba.
Gwiritsani ntchito nsinjiro zachiyankhulo, koma zisakhale koyambirira kwa ndime ndipo
zisatsangane
Musagwiritse ntchito mawu olaula ndi achipongwe
Lembani malembo ooneka bwino
Ndondomeko yophunzitsira chimangirizo mu sitandade 3 ndi 4
Pezani zitsanzo za ndondomeko m’buku la mphunzitsi la sitandade 3 ndi 4.
Ndondomeko yophunzitsira chimangirizo mu sitandade 5 mpaka 8
Lembani mutu wa chimangirizo pabolodi
Kambiranani ndi ophunzira mfundo zazikuluzikulu pa mutu omwe wasankhidwandi
kuzisanja mu ndondomeko yoyenera
Kambiranani ndi ophunzira chitsanzo cha momwe angalembere chimangirizo pogwiritsa
ntchito mafunso.
Ophunzira alembe chimangirizo pogwiritsa ntchito mutu omwe mwapereka potsatira
mafunso owatsogolera.
Onani ntchito ya ophunzira ndi kuwathandiza pamene akulemba
Pomaliza tengani ntchito ya ophunzira kuti mukachonge.
MUTU 11: Kaphunzitsidwe ka kulemba kalata
Ndondomeko yophunzitsira kulemba kalata ya ntchito m’sitandade 5 mpaka 8
Funsani ophunzira ngati adalembapo kapenaa kuwonapo kalata yantchito.
Pachikani tchati ya chitsanzo cha kalata yantchito ndipo mukambirane ndi ophunzira
magawo a kalata monga keyala, tsiku, komwe kalata ikupita, malonje, thunthu, mathero.
Ophunzira alembe kalata yantchito pa mutu omwe mwapereka ndipo mphunzitsi ayendere
ndi kuthandiza ophunzira.
Pomaliza, ophunzira ena angspo awerenge kalata zawo ndipo mutenge makope awo kuti
mukachonge.
MUTU 12: Kaphunzitsidwe ka kulmba nkhani, nthano ndi sewero
Mfundo zoyenera kutsata polemba nkhani, nthano ndi sewero
Kusankha mutu wosavuta kupeza mfundo zosangalatsa zikatambasulidwa
Mutu ukhale wolingana ndi nzeru za ophunzira
Osalemba mawu achipongwe kapena olaula
Malembo azikkhala owerengeka
Chiganizo chilichonse chizikhala ndi mfundo yayikulu
Mfundo yayikulu itambasulidwe mokwanira
Ndime ziziyalidwa mu dongosolo loyenera kutsatira kufunika kwake
Pa ndime iliyonse pazikhala mfundo yoomba mkota
Nthano, nkhani ndi sewero zizikhala zosangalatsa
Kuwerenga ndi kukonza zomwe zalembedwa
MUTU 13: Kaphunzitsidwe ka kugwiritsa ntchito malamulo a chiyankhulo
Zomwe zimalepheretsa ophunzira akupulayimale kugwiritsa ntchito malamulo achiyankhulo
moyenera.
Kusagwiritsa ntchito zipangizo pophunzitsa
Kusagwiritsa ntchito zipangizo zosiyanasiyana pophunzitsa
Kusakhala ndi chizoloweza chowerenga mabuku owonjezera nzeru
Chizolowezi choyankhula ziyankhulo zachilendo monga chingerezi
Chizolowezi choyankhula ziyankhulo zam’madera
Kusakhala ndi chidwi pa phunziroli
Njira zomwe zingathandize kuthetsa mavuto omwe ophunzira amakumana nawo pogwiritsa
ntchito malamulo a chiyankhulo.
Kugwiritsa ntchito zipangizo zoyeneraa pophunzitsa
Kutsata njira zosiyanasiyana pophunzitsa
Kukhala ndi chizolowezi chowerenga mabuku oonjezera
Kuzoloweraa kuyankhula Chichewa
Kukhala ndi chizolowezi choyankhula Chichewa chithyakuka
Kukhala ndi chidwi pa phunziroli
MUTU 14: Kaphunzitsidwe ka ndagi/zilapi
mitundu ya ndagi
Ndagi zonena zinthu zamoyo
Ndagi zonena zinthu zopanda moyo
Kufunika kwa ndagi.
Kuthandiza kuganiza mozama
Kubweretsa chisangalalo
Kusunga chikhalidwe chamakolo
Mutu 15: Kaphunzitsidwe ka mikuluwiko
Kufunika kwa mikuluwiko
Imakometsa nkhani
Imathandiza poyankhula mozimbaitsa
Imagwiritsidwa ntchito pa milandu
Imathandiza kuganiza mozama
Imaphunzitsa ndi kulimbikitsa makhalidwe abwino
Imaphunzitsa chiyambi cha zinthu
Imapititsa patsogolo chikhalidwe cha makolo
Imathandiza kuyanjanitsa anthu omwe asemphana mawu (akukangana)
Ndondomeko yophunzitsira mikuluwiko
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akudziwako zokhudza mikuluwiko
Kupereka tanthauzo la mkuluwiko
Kupereka zitsanzo za mikuluwiko
Kupereka matanthauzo ya mikuluwiko yomwe yaperekedwa ngati zitsanzo
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kulemba matanthauzo a mikuluwiko
Kuuza ophunzira kukachita kafukufuku wa zitsanzo zina za mikuluwiko.
Kufunika kwa nthano
Kusangalatsa
Kuphunzitsa
Kudziwitsa
Ndondomeko yophunzitisira nthano
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akudziwako zokhudza nthano
Kupereka tanthauzo la nthano
Kupereka chitsanzo cha nthano
Kunena nthano
Kufotokoza kapekedwe ka nthano
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kuyankha mafunso ndi kupereka phunziro lopezeka
mu nthano kapena kukamba za apangankhani, malo nthawi ndi zina.
Kuuza ophunzira kukachita kafukufuku wa zitsanzo zina za nthano.
Mutu 17: Kaphunzitsidwe ka sewero
Kufunika kwa phunziro la sewero
Kuyankhula pagulu mopanda manyazi
Kusangalatsa
Kupititsa patsogolo luso lomvetsera mwatcheru
Kuphunzitsa
Kuthandiza kuganiza mozama
Kukonzekera ntchito yodzagwira mtsogolo
Kudzudzula
Kidziwitsa anthu zinthu zosiyanasiyana
Ndondomeko yophunzitsira sewero
Kufunsa ophunzira kuti afotokoze zomwe akuzidziwa zokhudza sewero/zisudzo
Kupereka chitsanzo cha sewero
Kufotokoza kufunika kwa sewero
Kufotokoza zopezeka m’sewero
Kuchita sewero
Kupereka ntchito kwa ophunzira monga kuchita sewero, kufotokoza za atengambali,
makhalidwe awo, komamso phunziro lopezeka mu sewero.
Kuchita kafukufuku wa masewero ena.
Mutu 18: Kaphunzitsidwe ka kuzukuta (analysis of) nyimbo ndi ndakatulo
Mfundo zoyenera kutsatira pozukuta nyimbo kapena ndakatulo
Ndani akuyankhula?
Akuti chiyani?
Akuyankhula ndi yani?
N’chifukwa chiyani akuyankhula zimenezi?
Kodi woyankhulayo ndi wosangalala, wachisoni, wokhumudwa?
Ndi mfundo yayikulu iti yomwe ikupezeka mu nyimbo kapena ndakatulo
Zipangizo za nsetso (mawu apadera omwe amagwiritsidwa ntchito monga: mpeputso,
msemphano, voko, m’malere)
Njira zophunzitsira kumvetsa nkhani/nthano yomwe ophunzira awerenga.
Njira yolosera pogwiritsa ntchito mutu ndi zithunzi za nkhani/nthano
Ophunzira amafunsidwa mafunso pa mutu ndi zithunzi ndipo iwo amapereka maganizo awo
nkhani/nthano isanawerengedwe, monga mukuganizo kuti nkhaniyi ikamba zotani?
Lembani pa bolodi zina mwa zomwe ophunzira akuganiza.
Chepetsani mafunso oti “mukuonapo chiyani” pachithunzipa.
Njirayi imapereka chidwi kwa ophunzira chofuna kuwerenga nkhani.
Njira yolosera mathero a nkhani
Tikawerenga kapena kumvetsera ndime kapena gawo la nkhani timatha kulosera mathero a
nkhani.
Timafunsa mafunso monga: Kodi nkhaniyi itha bwanji malingana ndi ndime y(z)omwe
tawerenga kapena kumvetsera?
Njira yopanga chithunzithunzi cha nkhani
Tikamawerenga kapena kumvetsera nkhani timatha kupanga chithunzithunzi m’maganizo
mwathu cha zimene zikuchitika, malo kapena nthawi yomwe nkhani ikuchitika ndi omwe
akuchita.
Izi zimathandiza kumvetsa ndi kukumbukira zomwe zawerengedwa.
Njira yofotokozanso nkhani
Uku ndikufotokoza nkhani m’mawu athuathu momwe tayiwerengera ndi kuyimvetsera.
Njira yopanga mafunso
Timapanga mafunso tikatha kuwerenga nkhani.
Mafunso amakhala okhudza ampangankhani, malo, mfundo zikuluzikulu ndi phunziro
lopezeka m’nkhaniyo.
Njira yodzifunsa mafunso
Njirayi timadzifunsa mafunso pamene tikuwerenga nkhani.
Titha kufunsa mafunso tikawerenga mizere ingapo kapena ndime imodzi, monga: Kodi
munthuyu amakatani kumsikaku?
Njira younika mpangankhani
M’njirayi timapeza yemwe akuyankhula m’nkhani, zomwe akuyankhula ndi zifukwa zake,
gawo lomwe akutenga, ubale ndi ampangankhani ena komanso malo ndi nthawi yochitikira
nkhani.
Njira ya kalozera wa mfundo zikuluzikulu
Njirayi timayang’ana mfundo zikuluzikulu zomwe zikupezeka m’nkhani kapena m’macheza.
Njira yolumikiza zomwe akudziwa kale ndi zimene aphunzire.